PEMPHERO LOCHEZERANA (#13481)

*(Mapemphero 	ili 	limawerengedwa 	pa 	Manda 	a Bahá’u’lláh ndi Báb. Limagwiritsidwanso ntchito pokumbukira kubadwa kwa Bahá’u’lláh ndi Báb komanso kukumbukira kuwera kumwamba kwa Bahá’u’lláh ndi kuphedwa kwa Báb)  
 Mayamiko amene m’bandakucha wake waonekera ndi nkhope Yanu yolemekezeka kopambana, ndi ulemelero umene wawala kuchokera kwa Wokongola mowala kopambana, akhale pa Inu, O Inu Amene Muli Maonekedwe a Ulemelero, ndi Mfumu Yamuyaya, ndi Ambuye wa onse amene ali m’mwamba ndi padziko lapansi!  
Ine nditsimikiza kuti kupyolera mwa Inu Ufumu wa Mulungu ndi Ukulu wa Mulungu ndi Ulemelero Wake, zinabvumbulutsidwa, ndipo nthanda za kunyezimira Kwake kwakale-kale zagwetsa kuwala kwao kumwamba kwa lamulo Lanu losasinthika, ndipo kukongola kwa Wosaonekayo kwawala pamwamba pa zolengedwa zonse.  
Nditsimikizanso kuti ndi kuyenda kwa Cholembera Chanu Chokha, Chifuniro Chanu chakuti: “Khala Iwe” chakwaniritsidwa, ndiponso chinsinsi cha Mulungu chaululidwa, ndipo zinthu zonse zolengedwa zaitanidwa kumoyo ndi Zibvumbulutso zonse zatsika pansi.  
Ine ndichitira umboninso, kuti kupyolera mwa kukongola Kwanu, Kukongola kwa Wopembedzayo kwaonetsedwa, ndipo kupyolera mwa Nkhope Yanu, Nkhope ya Wofunikayo Yawala, ndi kuti kupyolera mwa mau Anu, Inu mwaganizira bwino pakati pa zolengedwa zonse, kuwapangitsa amene ali wopembedza Inu kukwera ku nsonga ya ulemelero, ndi wosakhulupilira kugwera m’mbuna yakuya.  
Ine ndichitira umboni kuti iye amene wakudziwani Inu wadziwa Mulungu, ndi iye amene wafika pamaso Panu wafika pamaso pa Mulungu. Chomwecho nkwakukulu kudalitsidwa kwa iye amene wakhulupilira mwa Inu, ndi mwa zizindikiro Zanu, ndipo walemekezedwa ndi kukomana Nanu, ndipo wafika pa zokoma za chifuniro Chanu, ndi kukuzungulirani ndi kuima patsogolo pa Mpando Wanu.  
Tsoka kwa iye amene wakulakwirani Inu, ndipo wakukanani Inu, ndipo sanabvomera zizindikiro Zanu, ndipo watsutsa ufumu Wanu, ndipo wakuukirani Inu, ndipo 	wasonyeza 	kunyada 	pamaso 	Panu, 	ndipo wakangana 	ndi 	maumboni 	Anu, 	ndipo 	wathawa chilamulo Chanu ndi ulamuliro Wanu ndi kuwerengedwa limodzi 	ndi 	wosakhulupilira 	amene 	maina 	awo asindikizidwa ndi zala za kulamula Kwanu pamauthenga Anu oyera.  
Chomwecho, uzirani kwa ine, O Mulungu wanga ndi Wokondedwa wanga, kuchokera kudzanja lamanja la chifundo Chanu ndi chisoni cha kukonda Kwanu, mphweya woyera wa ubwino Wanu, kuti zindichotse ine ndekha ndi m’dziko lapansi ndi kunditengera ku mabwalo a kuyandikira kwanu ndi pamaso Panu. Muli ndi mphamvu kuchita zomwe zakukomerani. Inu ndithudi Mwakhala Wamphamvu koposa zonse.  
Chikumbukiro cha Mulungu ndi mayamiko Ache, ndi Ulemelero wa Mulungu ndi kuwala kwake zikhale pa Inu, O Inu Amene Muli kukongola Kwake! Ndichitira umboni kuti diso la chilengedwe silinaone wina wolakwiridwa monga Inu. Munamizidwa masiku onse amoyo Wanu pansi pa nyanja ya zowawa. Pa nthawi yina Munali m’maunyolo 	ndi 	nsinga; 	pa 	nthawi 	yinanso Munaopsezedwa ndi lupanga la adani Anu. Komabe, ngakhale ziri chomwecho munalamulira wanthu onse kutsata zonse zimene Munalangizidwa ndi Iye Amene Ali Wodziwa Zonse, Wanzeru Zonse.  
Lolani mzimu wanga ukhale nsembe chifukwa cha zolakwa zimene Inu Munabvutika nazo ndi moyo wanga ukhale chopereka chifukwa cha mikwingwirima yomwe Munapwetekedwa nayo. Ndipempha Mulungu,mwa Inu ndi mwa iwo amene nkhope zawo zawalitsidwa ndi kuunika kwa Nkhope Yanu, ndi iwo amene, chifukwa cha chikondi Chanu, atsata zonse zimene anafunsidwa, kuchotsa zophimba zomwe zabwera pakati pa Inu ndi zolengedwa Zanu, ndi kundipatsa ine zabwino padziko lino ndi dziko lirinkudza. Inu zoonadi Ndinu 
Wamphamvu Zonse, Wam’mwamba-mwamba, Woyerayera, Wokhululukira Nthawi Zonse, Wachifundo Chozama.  
Dalitsani, 	O 	Ambuye 	Ambuye 	wanga, 	Mtengo Wopatulika wa Lote ndi masamba ake, ndi makungwa ake ndi nthambi zake, ndi misinde yake ndi mphukira zake malingana ndi momwe maina Anu opambana adzakhalira ndi maudindo Anu wotchuka kwambiri adzatha. Uchinjilizeni chomwecho kuchokera ku zokhumudwitsa za achiwembu ndi magulu ankhanza.  
Inu Ndinu, zoonadi Wamphamvu Zonse, Wolimba Kwambiri. Dalitsaninso, O Ambuye Mulungu wanga, antchito Anu ndi adzakazi Anu amene afika kwa Inu. Inu zoonadi Ndinu Wachifundo Chonse, amene chisomo Chake m’chamuyaya. Palibe Mulungu wina koma Inu, Wokhululukira-nthawi Zonse, Wokomamtima.

-`Abdu'l-Bahá
-----------------------

